Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine (Luka 9:23).
Kuti mukhale opambanadi ndi Ambuye, muyenera kuyenda mu nzeru zake. Mumuyike Iye akhale oyamba nkulola kuti nzeru zake zikutsogoleleni ponsepo. Mau a Mulungu ndi nzeru za Mulungu. Tsono, ikani chidwi chambiri pa Mau. “Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse...” Akolosi 3:16.
Zachisoni anthu ambiri amaziphunzitsa kukhazikika pa zosafunikazo chifukwa sadziwa kuti zofunikiradi ndi ziti. Amayika nthawi ndimphamvu zawo mu zinthu zimene siziwerengeredwa kumwamba. Zimakumbutsa nkhani ya azichemwali awiri, Marita ndi Maria, amene adachita mosiyana Yesu atawayendera ku nyumba kwawo (werengani Luka 10:38-42).
Marita anatanganidwa ndi ntchito zapakhomo zambirimbiri zolandira alendo, kuphatikiza chisangalalo ndi phuma zomusokoneza ndithu. Komatu, Maria adasankha kukhala pa mapazi a Yesu kuti alandire chiphunzitso chake nkumacheza naye, ndipo Ambuye adayamikira chisankho chakechi.
Pamene Marita adawonetsera kukhumudwa kwake, Ambuye adayankha modekha: “...Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri; koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye” (Luka 10:41-42). Ambuye adatsindika kuti Marita sadadziwe chofunikira kuposa zina.
Muyenera kuika patsogolo Mau a Mulungu kuposa zina zonse, chifukwa pali zambiri zimene simungadzadziwe kapena kuzimvetsa kopanda Mau. Ikani chidwi pa zinthu zimene ziri zofunikadi— kuwerenga ndi kulingalira kwanu pa Mau, komanso chiyanjano chanu ndi Mzimu Woyera. zikusungani pa njira ya ulemelero ochulukirachulukira, chigonjetso, kuchita bwino ndi chuma, ndipo mudzakhala moyo umene umamusangalatsa ndi kumulemekeza Ambuye.